Malawian National Anthem - Mulungu dalitsa Malaŵi lyrics
Songs
2024-12-29 12:46:55
Malawian National Anthem - Mulungu dalitsa Malaŵi lyrics
Mlungu dalitsani Malaŵi,
Mumsunge m'mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogoleri nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.
Malaŵi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N'mphatso zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malaŵi.
O Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malaŵi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n'chimodzi.
Mayi, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malaŵi.