Malawian National Anthem - Mulungu dalitsa Malaŵi [Portuguese translation]
Songs
2025-01-04 12:09:34
Malawian National Anthem - Mulungu dalitsa Malaŵi [Portuguese translation]
Mlungu dalitsani Malaŵi,
Mumsunge m'mtendere.
Gonjetsani adani onse,
Njala, nthenda, nsanje.
Lunzitsani mitima yathu,
Kuti tisaope.
Mdalitse Mtsogoleri nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.
Malaŵi ndziko lokongola,
La chonde ndi ufulu,
Nyanja ndi mphepo ya m'mapiri,
Ndithudi tadala.
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
N'mphatso zaulere.
Nkhalango, madambo abwino.
Ngwokoma Malaŵi.
O Ufulu tigwirizane,
Kukweza Malaŵi.
Ndi chikondi, khama, kumvera,
Timutumikire.
Pa nkhondo nkana pa mtendere,
Cholinga n'chimodzi.
Mayi, bambo, tidzipereke,
Pokweza Malaŵi.